Pakuti ndinacita manyazi kupempha kwa mfumu gulu la asilikari, ndi apakavalo, kutithandiza pa adani panjira; popeza tidalankhula ndi mfumu kuti, Dzanja la Mulungu wathu likhalira mokoma onse akumfuna; koma mphamvu yace ndi mkwiyo wace zitsutsana nao onse akumsiya.