Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 6:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo analamulira Dariyo mfumu, ndipo anthu anafunafuna m'nyumba ya mabuku mosungira cuma m'Babulo.

2. Napeza ku Akimeta m'nyumba ya mfumu m'dera la Mediya, mpukutu, ndi m'menemo munalembedwa motere, cikhale cikumbutso:

3. Caka coyamba ca Koresi mfumu, analamulira Koresi mfumuyo, Kunena za nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, imangidwe nyumbayi pamalo pophera nsembe, namangidwe kolimba maziko ace, msinkhu wace mikono makumi asanu ndi limodzi, kupingasa kwace mikono makumi asanu ndi limodzi;

4. ndi mipambo itatu ya miyala yaikuru, ndi mpambo wa mitengo yatsopano; nalipidwe ndarama zocokera ku nyumba ya mfumu.

5. Ndi zipangizo za golidi ndi siliva za nyumba ya Mulungu, zimene anaziturutsa Nebukadinezara m'Kacisi ali ku Yerusalemu, nazitenga kumka nazo ku Babulo, azibwezere, nabwere nazo ku Kacisi ali ku Yerusalemu, ciri conse ku malo ace; naziike m'nyumba ya Mulungu.

6. Tsono iwe, Tatinai, kazembe wa tsidya lija la mtsinjewo, Setara Bozenai, ndi anzanu Afarisikai, okhala tsidya lija la mtsinje, muzikhala kutali;

7. lekani nchito iyi ya Mulungu, osaibvuta; kazembe wa Ayuda ndi akulu a Ayuda amange nyumba iyi ya Mulungu pambuto pace.

8. Ndilamuliranso za ici muzicitira akuru awa a Ayuda, kuti amange nyumba iyi ya Mulungu, ndiko kuti mutengeko cuma ca mfumu, ndico msonkho wa tsidya la mtsinje, nimupereke zolipira kwa anthu awa msanga, angawacedwetse.

9. Ndipo zosowa zao, ana a ng'ombe, ndi nkhosa zamphongo, ndi ana a nkhosa, zikhale nsembe zopsereza za Mulungu wa Kumwamba; tirigu, mcere, vinyo, mafuta, monga umo adzanena ansembe ali ku Yerusalemu, ziperekedwe kwa iwo tsiku ndi tsiku, zisasoweke;

10. kuti apereke nsembe zonunkhira bwino kwa Mulungu wa Kumwamba, napempherere moyo wa mfumu ndi wa ana ace.

11. Ndalamuliranso kuti ali yense adzasintha mau awa, usololedwe mtanda kunyumba kwace, namkweze, nampacike pomwepo; niyesedwe dzala nyumba yace cifukwa ca ici;

12. ndipo Mulungu wokhalitsa dzina lace komweko agwetse mafwnu onse ndi mitundu yonse ya anthu, akuturutsa dzanja lao kusintha mau awa, kuononga nyumba ya Mulungu iri ku Yerusalemu. Ine Dariyo ndalamulira, cicitike msanga.

13. Pamenepo Tatinai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, Setara Bozenai, ndi anzao, popeza mfumu Dariyo adatumiza mau, anacita momwemo cofulumira.

14. Ndipo akulu a Ayuda anamanga opanda cosoweka, mwa kunenera kwa mneneri Hagai, ndi Zekariya mwana wa Ido. Naimanga, naitsiriza, monga mwa lamulo la Mulungu wa Israyeli, ndi monga mwa lamulo la Koresi, ndi Dariyo, ndi Aritasasta mfumu ya Perisiya,

Werengani mutu wathunthu Ezara 6