Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 3:2-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Nanyamuka Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ace ansembe, ndi Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ndi abale ace, namanga guwa la nsembe la Mulungu wa Israyeli, kuperekapo nsembe zopsereza, monga mulembedwa m'cilamulo ca Mose munthu wa Mulungu.

3. Ndipo anakhazika guwa la nsembe patsinde pace cifukwa ca kuopa iwo anthu a m'maikomo; nakwezera Yehova nsembe zopsereza pamenepo, nsembe zopsereza zam'mawa ndi zamadzulo.

4. Nacita madyerero a misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ace, monga mwa lamulo lace la tsiku lace pa tsiku lace;

5. atatero anaperekanso nsembe yopsereza yosalekeza, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika zonse za Yehova zopatulika, ndi za munthu yense wopereka nsembe yaufulu kwa Yehova mwaufulu.

6. Ciyambire tsiku loyamba la mwezi wacisanu ndi ciwiri anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova; koma sanamange maziko a Kacisi wa Yehova.

7. Anaperekanso ndarama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi cakudya, ndi cakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Turo, kuti atenge mikungudza ku Lebano, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Koresi mfumu ya Babulo.

8. Caka caciwiri tsono cakufika iwo ku nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, mwezi waciwiri, Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi ndi onse ocokera kundende kudza ku Yerusalemu, anayamba, naika Alevi a zaka makumi awiri ndi mphambu, ayang'anire nchito ya nyumba ya Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezara 3