Anaperekanso ndarama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi cakudya, ndi cakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Turo, kuti atenge mikungudza ku Lebano, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Koresi mfumu ya Babulo.