Ndipo anakhazika guwa la nsembe patsinde pace cifukwa ca kuopa iwo anthu a m'maikomo; nakwezera Yehova nsembe zopsereza pamenepo, nsembe zopsereza zam'mawa ndi zamadzulo.