Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 8:21-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Pakuti ukapanda kulola anthu anga amuke, taona, ndidzatuma mizaza pa iwe, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba zako; ndipo nyumba za Aaigupto zidzadzala nayo mizaza, ndi nthaka yomwe imene ikhalapo.

22. Ndipo tsiku ilo ndidzalemba malire dziko la Goseni, m'mene mukhala anthu anga, kuti pamenepo pasakhale mizaza; kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova pakati pa dzikoli.

23. Ndipo ndidzaika cosiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako; mawa padzakhala cizindikilo ici.

24. Ndipo Yehovaanacita comweco; ndipo kunafika magulu a mizaza m'nyumba ya Farao, ndi m'nyumba za anyamata ace, ndi m'dziko lonse la Aigupto; dziko linaipatu cifukwa ca mizazayo.

25. Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mukani, mphereni nsembe Mulungu wanu m'dzikomu.

26. Koma Mose anati, Sikuyenera kutero; pakuti tidzamphera Yehova Mulungu wathu conyansa ca Aaigupto; taonani, ngati tikamphera nsembeconyansaca Aaigupto pamaso pao sadzatiponya miyala kodi?

27. Timuke ulendo wa masiku atatu m'cipululu, tikamphere Yehova Mulungu wathu nsembe, monga adzanena nafe.

28. Ndipo Farao anati, Ndidzakulolani mumuke, kuti mukamphere nsembe Yehova. Mulungu wanu m'cipululu; komatu musamuke kutaritu: mundipembere.

29. Ndipo Mose anati, Onani, ndirikuturuka ine kwanu, ndidzapemba Yehova kuti mizaza icoke mawa kwa Farao, ndi kwa anyamata ace, ndi kwa anthu ace; komatu, Farao asanyengenso ndi kukana kulola anthuwa amuke kukamphera nsembe Yehova.

30. Ndipo Mose anaturuka kwa Farao, napemba Yehova.

31. Ndipo Yehova anacita monga mwa mau a Mose; nacotsera Farao ndi anyamata ace ndi anthu ace mizazayo, sunatsala ndi umodzi wonse.

32. Koma Farao anaumitsa mtima wace nthawi yomweyonso, ndipo sanalola anthu amuke.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 8