Pakuti ukapanda kulola anthu anga amuke, taona, ndidzatuma mizaza pa iwe, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba zako; ndipo nyumba za Aaigupto zidzadzala nayo mizaza, ndi nthaka yomwe imene ikhalapo.