Ndipo Mose anati, Onani, ndirikuturuka ine kwanu, ndidzapemba Yehova kuti mizaza icoke mawa kwa Farao, ndi kwa anyamata ace, ndi kwa anthu ace; komatu, Farao asanyengenso ndi kukana kulola anthuwa amuke kukamphera nsembe Yehova.