Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 8:14-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo anawaola miulu-miulu; ndi dziko linanunkha.

15. Koma pamene Farao, anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wace, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.

16. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande pfumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m'dziko lonse la Aigupto.

17. Ndipo anacita comweco; pakuti Aroni anasamula dzanja lace ndi ndodo yace, napanda pfumbi lapansi, ndipo panali nsabwe pa anthu ndi pa zoweta; pfumbi lonse lapansi liinasanduka nsabwe m'dziko lonse la Aigupto.

18. Alembi anateronso ndi matsenga ao kuonetsa nsabwe, koma sanakhoza; ndipo panali nsabwe pa anthu, ndi pa zoweta.

19. Pamenepo alembi anati kwa Farao, Cala ca Mulungu ici; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.

20. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uuke ulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao; taona, aturuka kumka kumadzi; nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, anditumikire.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 8