9. Ndipo Mose ananena comweco ndi ana a Israyeli; koma sanamvera Mose cifukwa ca kuwawa mtima, ndi ukapolo wolemera.
10. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
11. Lowa, lankhula ndi Farao mfumu ya Aigupto, kuti alole ana a Israyeli aturuke m'dziko lace.
12. Koma Mose ananena pamaso pa Mulungu, ndi kuti, Onani, ana a Israyeli sanandimvera ine; adzandimvera bwanji Farao, ndine wa milomo yosadula?
13. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nawalangiza za ana a Israyeli, ndi za Farao mfumu ya Aigupto, kuti aturutse ana a Israyeli m'dziko la Aigupto.
14. Akuru a mbumba za makolo ao ndi awa: ana amuna a Rubeni, woyamba wa Israyeli ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezroni, ndi Karmi; amene ndiwo mabanja a Rubeni.
15. Ndi ana amuna a Simeoni ndiwo: Yemweli, ndi Yamini, ndi Ohadi, Yakini, ndi Zohari, ndi Sauli mwana wa mkazi wa m'Kanani; amene ndiwo mabanja a Simeoni.
16. Ndipo maina a ana amuna a Levi, mwa kubadwa kwao ndiwo: Gerisoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.
17. Ana amuna a Gerisoni ndiwo: Libni ndi Simei, mwa mabanja ao.