Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 4:20-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Pamenepo Mose anatenga mkazi wace ndi ana ace amuna, nawakweza pa buru, nabwerera kumka ku dziko la Aigupto; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lace.

21. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kumka ku Aigupto, usamalire ucite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wace kuti asadzalole anthu kupita.

22. Pamenepo ukanene ndi Farao, Atero Yehova, Mwana wanga, mwana wanga woyamba ndiye Israyeli.

23. Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba.

24. Ndipo kunali panjira, kucigono, Yehova anakomana naye, nafuna kumupha.

25. Koma Zipora anatenga mpeni wamwala, nadula khungu la mwana wace, naliponya pa mapazi ace; nati, Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi. Ndipo iye anamleka.

26. Pamenepo anati mkaziyo, Mkwati wamwazi iwe, cifukwa ca mdulidwe.

27. Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Muka kucipululu kukakomana ndi Mose. Ndipo anamuka, nakomana naye pa phiri la Mulungu, nampsompsona.

28. Ndipo Mose anauza Aroni mau onse a Yehova amene adamtuma nao, ndi zizindikilo zonse zimene adamlamulira.

29. Pamenepo Mose ndi Aroni anamuka nasonkhanitsa akuru onse a ana a Israyeli;

30. ndipo Aroni anawafotokozera mau onse amene Yehova adauza Mose, nacita zizindikilo zija pamaso pa anthu.

31. Ndipo anthuwo anakhulupirira; ndipo pamene anamva kuti Yehova adawazonda ana a Israyeli, ndi kuti adaona mazunzo ao, anawerama, nalambira Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 4