Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 4:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Mose anayankha nati, Koma taonani, sadzakhulupirira ine, kapena kumvera mau anga; pakuti adzanena, Yehova sanakuonekera iwe.

2. Ndipo Yehova ananena naye, Ico nciani m'dzanja lako? Nati, Ndodo.

3. Ndipo ananena iye, Iponye pansi. Naiponya pansi, ndipo inasanduka njoka; ndipo Mose anaithawa.

4. Koma Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako, nuigwire kumcira; ndipo anatambasula dzanja lace, naigwira, nikhalanso ndodo m'dzanja lace;

5. kuti akhulupirire kuti wakuonekera Yehova Mulungu wa makolo ao, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.

6. Ndipo Yehova ananenanso naye, Longa dzanja lako pacifuwa pako. Ndipo analonga dzanja lace pacifuwa pace, naliturutsa, taonani, dzanja lace linali lakhate, lotuwa ngati cipale cofewa.

7. Ndipo ananena iye, Bwerezanso dzanja lako pacifuwa pako. Ndipo anabwerezanso dzanja lace pacifuwa pace; naliturutsa pacifuwa pace, taonani, linasandukanso lomwe lakale.

8. Ndipo kudzatero, ngati sakhulupirira iwe, ndi kusamvera mau a cizindikilo coyamba, adzakhulupirira mau a cizindikilo cotsirizaci.

9. Ndipo kudzatero, aka panda kukhulupirira zingakhale zizindikilo izi, ndi kusamvera mau ako, ukatunge madzi a kunyanja, ndi kuthira pamtunda; ndi madzi watunga ku nyanjayo adzasanduka mwazi pamtunda.

10. Ndipo Mose anati kwa Yehova, Mverani, Ambuye, ine ndine munthu wosowa ponena, kapena dzulo, kapena kale, kapena cilankhulire Inu ndi kapolo wanu, pakuti ndine wa m'kamwa molemera, ndi wa lilime lolemera.

11. Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu m'kamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Si ndine Yehova kodi?

12. Ndipo tsopano muka, ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi kukuphunzitsa comwe ukalankhule.

13. Koma anati, Mverani, Ambuye, tumizani pa dzanja la iye amene mudzamtuma.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 4