Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 38:20-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndi ziciri zonse za cihema, ndi za bwalo lace pozungulira, nza mkuwa.

21. Ici ndi ciwerengo ca zinthu za cihema, cihema ca mboni, monga anaziwerenga, monga mwa mau a Mose, acite nazo Alevi; anaziwerenga Itamara, mwana wa Aroni wansembe.

22. Ndipo Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa pfuko la Yuda, anapanga zonse zimene Mulungu adauza Mose.

23. Ndi pamodzi naye Aholiabu, mwana wa Ahisama, wa pfuko la Dani, ndiye wozokota miyala, ndi mmisiri waluso, ndiponso wopikula ndi lamadzi ndi lofiira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

24. Golidi yense anacita naye mu nchito yonse ya malo opatulika, golidi wa coperekaco, ndico matalente makumi awiri kudza asanu ndi anai, ndi masekeli mazana asanu ndi awiri, kudza makumi atatu, monga mwa sekeli wa malo opatulika.

25. Ndipo siliva wa iwo owerengedwa a khamulo ndiwo matalente zana limodzi, ndi masekeli cikwi cimodzi, kudza mazana asanu ndi awiri, mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika;

Werengani mutu wathunthu Eksodo 38