Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 36:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Aholiabu, ndi anthu aluso, amene Yehova adaika luso ndi nzeru m'mtima mwao adziwe macitidwe ace a nchito yonse ya utumiki wace wa malo opatulika, monga mwa zonse adauza Yehova.

2. Ndipo Mose adaitana Bezaleli ndi Aholiabu, ndi anthu onse aluso, amene Yehova adaika luso m'mtima mwao, onse ofulumidwa mtima ayandikize kunchito kuicita.

3. Ndipo analandira kwa Mose copereka conse, cimene ana a Israyeli adabwera naco cikhale ca macitidwe a nchito ya malo opatulika, aipange naco. Koma anaonjeza kubwera nazo kwa iye zopereka zofuna mwini, m'mawa ndi m'mawa.

4. Ndipo aluso onse, akucita nchito yonse ya malo opatulika, anadza onse ndi kusiya nchito yao: analinkucita;

5. nanena ndi Mose, ndi kuti, Anthu alinkubwera nazo zocuruka, zakuposera zoyenera nchito imene Yehova anauza icitike.

6. Ndipo Mose analamulira, ndipo anamveketsa mau mwa cigono conse, ndi kuti, Asaonjezere nchito ya ku copereka ca malo opatulika, ngakhale mwamuna ngakhale mkazi. Tero anawaletsa anthu asabwere nazo zina.

7. Popeza zipangizo zinakwanira nchito yonse icitike, zinatsalakonso.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 36