Ndipo Mose analamulira, ndipo anamveketsa mau mwa cigono conse, ndi kuti, Asaonjezere nchito ya ku copereka ca malo opatulika, ngakhale mwamuna ngakhale mkazi. Tero anawaletsa anthu asabwere nazo zina.