Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 32:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma pamene anaona kuti Mose anacedwa kutsika m'phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kucokera m'dziko la Aigupto, sitidziwa comwe camgwera.

2. Ndipo Aroni ananena nao, Thyolani mphete zagolidi ziri; m'makutu a akazi anu, a ana anu amuna ndi akazi, ndi kubwera nazo kwa ine.

3. Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolidi zinali m'makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni.

4. Ndipo anazilandira ku manja ao, nacikonza ndi cozokotera, naciyenga mwana wa ng'ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israyeli, imene inakukweza kucokera m'dziko la Aigupto.

5. Pakuciona Aroni, anamanga guwa la nsembe patsogolo pace; ndipo Aroni anapfuula nati, Mawa aliko madyerero a Yehova.

6. Ndipo m'mawa mwace anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera.

7. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nao kucokera m'dziko la Aigupto wadziipsa;

8. wapatuka msanga njira imene ndinawauza; wadzinyengera mwana wa ng'ombe, namgwadira, namphera nsembe, nati, Siyi milungu yako, Israyeli, imene inakukweza kucokera m'dziko la Aigupto,

9. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ndawapenya anthu awa, taona, ndiwo anthu opulupudza;

10. ndipo tsopano ndileke, kuti ndipse mtima pa awo ndi kuwatha, ndi kukuza iwe ukhale mtundu waukuru.

11. Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wace, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawaturutsa m'dziko la Aigupto ndi mphamvu yaikuru, ndi dzanja lolimba?

12. Akaneneranji Aaigupto; ndi kuti, Anawaturutsa coipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope pa dziko lapansi? Pepani, lekani coipaco ca pa anthu anu.

13. Kumbukilani Abrahamu, Isake ndi Israyeli, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzichula nokha, amene munanena nao, Ndidzacurukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale colowa cao nthawi zonse.

14. Ndipo Yehova analeka coipa adanenaci, kuwacitira anthu ace.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 32