Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 3:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wace, wansembe wa ku Midyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa cipululu, nafika ku phiri la Mulungu, ku Horebe.

2. Ndipo mthenga wa Molungu anamuonekera m'cirangali camoto coturuka m'kati mwa citsamba; ndipo anapenya, ndipo taonani, citsamba cirikuyaka moto, koma cosanyeka citsambaco.

3. Ndipo Mose anati, Ndipatuketu, ndikaone cooneka cacikuruco, citsambaco sicinyeka bwanji,

4. Pamene Yehova anaona kuti adapatuka kukapenya, Mulungu ali m'kati mwa citsamba, anamuitana, nati, Mose, Mose. Ndipo anati, Ndiri pano.

5. Ndipo iye anati, Usayandikire kuno; bvula nsapato zako ku mapazi ako, pakuti pamalo pamene upondapo iwe, mpopatulika.

6. Ananenanso Ine ndine Mulungu wa atate wako, Molungu wa Abrahamu, Molungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Mose anabisa nkhope yace; popeza anaopa kuyang'ana Mulungu,

7. Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali m'Aigupto, ndamvanso kulira kwao cifukwa ca akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;

8. ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Aigupto, ndi kuwatumtsa m'dziko lila akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikuru, m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.

9. Ndipo tsopano, taona kulira kwa ana a Israyeli kwandifikira; ndapenyanso kupsinjika kumene Aaigupto awapsinja nako.

10. Tiye tsopano, ndikutuma kwa Farao, kuti uturutse anthu anga, ana a Israyeli m'Aigupto.

11. Koma Mose anati kwa Mulungu, Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao, ndi kuti nditurutse ana a Israyeli m'Aigupto?

12. Ndipo iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ici ndi cizindikilo ca iwe, cakuti ndakutuma ndine; utaturutsa anthuwo m'Aigupto mudzatumikira Mulungu paphiri pano.

13. Ndipo Mose anati kwa Mulungu, Onani, pakufika ine kwa ana a Israyeli, ndi kunena nao, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lace ndani? ndikanena nao ciani?

14. Ndipo Molungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDIRI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israyeli, INE NDINE wandituma kwa inu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 3