Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 28:27-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Upangenso mphete ziwiri zagolidi, ndi kuzimanga pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'munsi, ku mbali yace ya kutsogolo, pafupi pa msoko wace, pamwamba pa mpango wa efodi.

28. Ndipo amange capacifuwa pa mphete zace ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti cikhale pa mpango wa efodi; ndi kuti capacifuwa cisamasuke paefodi,

29. Ndipo Aroni azinyamula maina a ana a Israyeli pa capacifuwa ca ciweruzo pamtima pace, pakulowa iye m'malo opatulika, akhale cikumbutso pankhope pa Yehova kosalekeza.

30. Ndipo uike Urimu ndi Tumimu mwa capacifuwa ca ciweruzo; ndipo zikhale pa mtima wa Aroni, pakulowa iye pamaso pa Yehova; ndipo Aroni azinyamula ciweruzo ca ana a Israyeli pamtima pace pamaso pa Yehova kosalekeza.

31. Ndipo uombe mwinjiro wa efodi ndi lamadzi lokha.

32. Ndipo polowa mutu pakhale pakati pace; pakhale mkawo pozungulira polowa pace, wa nchito yoomba, ngati polowa pa malaya ociniiriza, pangang'ambike.

33. Ndipo pa mbinyiru wace upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiirira, pambinyiru pace pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolidi pozungulira;

34. mliu wagolidi ndi khangaza, mliu wagolidi ndi khangaza, pa mbinyiru wa mwinjiro pozungulira.

35. Ndipo Aroni aubvale kuti atumikire nao; ndipo limveke liu lace pakulowa iye m'malo opatulika pamaso pa Yehova, ndi pakuturuka iye, kuti asafe.

36. Ndipo upange golidi waphanthiphanthi woona, ndi kulocapo, monga malocedwe a cosindikizira. KUPATULIKIRA YEHOVA.

37. Nuciike pamkuzi wamadzi, ndipo cikhale panduwira, cikhale patsogolo pace pa nduwira.

38. Ndipo cizikhala pamphumi pace pa Aroni, ndipo Aroni azinyamula mphulupulu ya zopatulidwa, zimene ana a Israyeli azipatulira, ndi zopereka zao zonse zopatulira; ndipo cizikhala pamphumi pace kosalekeza, kuti alandiridwe pamaso pa Yehova.

39. Ndipo upikule maraya am'kati abafuta a thonje losansitsa, nusoke nduwira wabafuta, nusokenso mpango wopikapika.

40. Ndipo usokere ana a Aroni maraya am'kati, nuwasokere mipango; uwasokerenso akapa akhale aulemerero ndi okoma.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 28