Ndipo ubveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ace omwe; ndi a kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andicitire Ine nchito ya nsembe.