9. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akubvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo.
10. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zobvala zao,
11. nakonzekeretu tsiku lacitatu; pakuti tsiku lacitatu Yehova adzatsika pa phiri la Sinai pamaso pa anthu onse.
12. Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzicenjera musakwere m'phiri, musakhudza cilekezero cace; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu;
13. dzanja liri lonse lisalikhudze, wakulikhudza azimponyatu miyala, kapena kumpyoza; ngakhale coweta ngakhale munthu, zisakhale ndi moyo. Pamene lipenga libanika liu lace azikwera m'phirimo.
14. Ndipo Mose anatsika m'phiri kumka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zobvala zao.
15. Ndipo anati kwa anthu, Mukonzekeretu tsiku lacitatu nimusayandikiza mkazi.