Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 19:2-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Pakuti anacoka ku Refidimu, nalowa m'cipululu ca Sinai, namanga tsasa m'cipululumo; ndipo Israyeli anamanga tsasa pamenepo pandunji pa phirilo.

3. Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m'phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israyeli, kuti,

4. Inu munaona cimene ndinacitira Aaigupto; ndi kuti ndanyamula inu monga pa mapiko a mphungu, ndi kubwera nanu kwa Ine ndekha.

5. Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusunga cipangano canga, ndidzakuyesani cuma canga ca padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa;

6. ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a lsrayeli.

7. Ndipo Mose anadza, naitana akuru a anthu, nawaikira pamaso pao mau awa onse amene Yehova adamuuza.

8. Ndipo anthu onse anabvomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazicita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 19