Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 19:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mwezi wacitatu ataturuka ana a Israyeli m'dziko la Aigupto, tsiku lomwelo, analowa m'cipululu ca Sinai.

2. Pakuti anacoka ku Refidimu, nalowa m'cipululu ca Sinai, namanga tsasa m'cipululumo; ndipo Israyeli anamanga tsasa pamenepo pandunji pa phirilo.

3. Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m'phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israyeli, kuti,

4. Inu munaona cimene ndinacitira Aaigupto; ndi kuti ndanyamula inu monga pa mapiko a mphungu, ndi kubwera nanu kwa Ine ndekha.

5. Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusunga cipangano canga, ndidzakuyesani cuma canga ca padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa;

6. ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a lsrayeli.

7. Ndipo Mose anadza, naitana akuru a anthu, nawaikira pamaso pao mau awa onse amene Yehova adamuuza.

8. Ndipo anthu onse anabvomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazicita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.

9. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akubvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 19