Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 17:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli linacoka m'cipululu ca Sini, m'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona m'Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.

2. Pamenepo anthu anatsutsana ndi Mose, nati, Tipatseni madzi timwe, Koma Mose ananena nao, Mutsutsana nane bwanji? Muyeseranji Yehova?

3. Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kucokera ku Aigupto, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu?

4. Ndipo Mose anapfuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwacitenji anthuwa? andilekera pang'ono kundiponya miyala.

5. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pita pamaso pa anthu, nutenge pamodzi nawe akuru ena a Israyeli; nutenge m'dzanja mwako ndodo ija unapanda nayo nyanja, numuke.

6. Taona, ndidzaima pamaso pako pathanthwe m'Horebe; ndipo upande thanthwe, nadzaturukamo madzi, kuti anthu amwe. Ndipo Mose anacita comweco pamaso pa akuru a Israyeli.

7. Ndipo anacha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, cifukwa ca kutsutsana kwa ana a Israyeli; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai?

8. Pamenepo anadza Amaleki, nayambana ndi Israyeli m'Refidimu.

9. Ndipo Mose anati kwa Yoswa, Utisankhulire amuna, nuturuke kuyambana naye Amaleki; mawa ndidzaima pamwamba pa citunda, ndi ndodo ya Mulungu m'dzanja langa.

10. Ndipo Yoswa anacita monga Mose adanena naye, nayambana ndi Amaleki; ndipo Mose, ndi Aroni, ndi Huri anakwera pamwamba pa citunda.

11. Ndipo kunakhala, pamene Mose anakweza dzanja lace Israyeli analakika; koma pamene anatsitsa dzanja lace Amaleki analakika.

12. Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ace, wina mbali yina, wina mbali yina; ndi manja ace analimbika kufikira litalowa dzuwa.

13. Ndipo Yoswa anatyola Amaleki ndi anthu ace ndi kuukali kwa lupanga.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 17