Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 13:4-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Muturuka lero lino mwezi wa Abibu.

5. Ndipo kudzakhala atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, ndi la Ahiti, ndi la Aamori ndi la Ahivi, ndi la Ayebusi, limene analumbira ndi makolo ako kukupatsa, m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi, uzikasunga kutumikira kumeneku mwezi uno.

6. Masiku asanu ndi awiri uzikadya mkate wopanda cotupitsa, ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri likhale la madyerero a Yehova.

7. Azikadya mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiriwo ndipo kasaoneke kanthu ka cotupitsa kwanu; inde cotupitsa cisaoneke kwanu m'malire ako onse.

8. Ndipo ukauze mwana wako wamwamuna tsikulo, ndi kuti, Nditero cifukwa comwe Yehova anandicitira ine poturuka ine m'Aigupto,

9. Ndipo cizikhala ndi iwe ngati cizindikilo pa dzanja lako, ndi cikumbutso pakati pa maso ako; kuti cilamulo ca Yehova cikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakuturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu.

10. Cifukwa cace uzikasunga lemba ili pa nyengo yace caka ndi caka.

11. Ndipo kudzakhala, atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, monga anakulumbirira iwe ndi makolo ako, ndipo anakupatsa ilo,

12. kuti uzikapatulira Yehova onse oyamba kubadwa ndi oyamba onse uli nao odzera kwa zoweta; amunawo ndi a Yehova.

13. Koma woyamba yense wa buru uzimuombola ndi mwana wa nkhosa; ndipo ukapanda kumuombola uzimthyola khosi; koma oyamba onse a munthu mwa ana ako uziwaombola.

14. Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ici nciani? ukanene naye, Yehova anatiturutsa m'Aigupto, m'nyumba ya aka polo, ndi dzanja lamphamvu;

Werengani mutu wathunthu Eksodo 13