Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 12:16-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lacisanu ndi ciwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasacitike nchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzicita.

17. Ndipo muzisunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa; pakuti tsiku lomwe lino ndinaturutsa makamu anu m'dziko la Aigupto; cifukwa cace muzisunga tsiku lino m'mibadwo yanu, lemba losatha.

18. Mwezi woyamba, tsiku lace lakhumi ndi cinai madzulo ace, muzidya mkate wopanda cotupitsa, kufikira tsiku la makumi awiri mphambu limodzi la mwezi, madzulo ace.

19. Cisapezeke cotupitsa m'nyumba zanu masiku asanu ndi awiri; pakuti ali yense wakudya kanthu ka cotupitsa, munthuyo adzasadzidwa ku msonkhano wa Israyeli, angakhale ndiye mlendo kapena wobadwa m'dziko.

20. Musadye kanthu ka cotupitsa; mokhala inu monse muzidya mkate wopandacotupitsa.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 12