Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lacisanu ndi ciwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasacitike nchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzicita.