Ndipo muzisunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa; pakuti tsiku lomwe lino ndinaturutsa makamu anu m'dziko la Aigupto; cifukwa cace muzisunga tsiku lino m'mibadwo yanu, lemba losatha.