Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 10:12-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako pa dziko la Aigupto, lidze dzombe, kuti likwere pa dziko la Aigupto, lidye zitsamba zonse za m'dziko, ndizo zonse adazisiya matalala.

13. Pamenepo Mose analoza ndodo yace pa dziko la Aigupto; ndipo Yehova anaombetsa padziko mphepo ya kum'mawa usana wonse, ndi usiku womwe; ndipo kutaca mphepo ya kum'mawa inadza nalo dzombe.

14. Ndipo dzombe linakwera pa dziko lonse la Aigupto, ndipo linatera pakati pa malire onse a Aigupto, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere.

15. Pakuti linakuta nkhope ya dziko lonse kuti dziko linada; ndipo linadya zitsamba zonse za m'dziko, ndi zipatso zonse za mitengo zimene matalala adazisiya; ndipo sipanatsala cabiriwiri ciri conse, pamitengo kapena pa zitsamba za kuthengo, m'dziko lonse la Aigupto.

16. Pamenepo Farao anafulumira kuitana Mose ndi Aroni; nati, Ndalakwira Yehova Mulungu wanu, ndi inu.

17. Ndipo tsopano, ndikhululukirenitu kulakwa kwanga nthawi yino yokha, nimundipembere kwa Yehova Mulungu wanu, kuti andicotsere imfa yino yokha.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 10