Pamenepo Mose analoza ndodo yace pa dziko la Aigupto; ndipo Yehova anaombetsa padziko mphepo ya kum'mawa usana wonse, ndi usiku womwe; ndipo kutaca mphepo ya kum'mawa inadza nalo dzombe.