Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako pa dziko la Aigupto, lidze dzombe, kuti likwere pa dziko la Aigupto, lidye zitsamba zonse za m'dziko, ndizo zonse adazisiya matalala.