Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 9:21-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo ndinatenga cimo lanu, mwana wa ng'ombe mudampangayo, ndi kumtentha ndi moto, ndi kumphwanya, ndi kumpera bwino kufikira atasalala ngati pfumbi; ndipo ndinataya pfumbi lace m'mtsinje wotsika m'phirimo.

22. Ku Tabera, ndi ku Masa, ndi ku Kibiroti Hatava, munautsanso mkwiyo wa Yehova.

23. Ndipo pamene Yehova anakutumizani kucokera ku Kadesi Barinea, ndi kuti, Kwerani, landirani dziko limene ndakupatsani; munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu, osamkhulupirira, kapena kumvera mau ace.

24. Munakhala opikisana ndi Yehova kuyambira tsikuli ndinakudziwani.

25. Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova masiku makumi anai usana ndi usiku ndinagwa pansiwa; popeza Yehova adati kuti adzakuonongani.

26. Ndipo ndinapemphera kwa Yehova ndi kuti, Yehova Mulungu, musaononga anthu anu ndi colowa canu, amene mudawaombola mwa ukulu wanu, amene munawaturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu,

27. Kumbukilani atumiki anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo; musapenyerera kupulukira kwa anthu awa, kapena coipa cao, kapena cimo lao;

28. kuti linganene dziko limene mudatiturutsako, Popeza Yehova sanakhoza kuwalowetsa m'dziko limene adanena nao, ndi popeza anadana nao, anawaturutsa kuti awaphe m'cipululu.

29. Koma iwo ndiwo anthu anu ndi colowa canu, amene mudaturutsa ndi mphamvu yanu yaikuru ndi dzanja lanu lotambasuka.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 9