Ndipo ndinapemphera kwa Yehova ndi kuti, Yehova Mulungu, musaononga anthu anu ndi colowa canu, amene mudawaombola mwa ukulu wanu, amene munawaturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu,