Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 9:15-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Pamenepo ndinatembenuka ndi kutsika m'phiri, ndi phirilo linatentha ndi moto; ndi magome awiri a cipangano anali m'manja mwanga.

16. Ndipo ndinapenya, taonani, mudacimwira Yehova Mulungu wanu; mudadzipangira mwana wa ng'ombe woyenga; mudapatuka msanga m'njira imene Yehova adalamulira inu.

17. Pamenepo ndinagwira magome awiriwo, ndi kuwataya acoke m'manja anga awiri, ndi kuwaswa pamaso panu.

18. Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova, monga poyamba paja, masiku makumi anai usana ndi usiku, osadya mkate osamwa madzi, cifukwa ca macimo anu onse mudacimwa, ndi kucita coipaco pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wace.

19. Pakuti ndinacita mantha cifukwa ca mkwiyo waukali, umene Yehova anakwiya nao pa inu kukuonongani, Koma Yehova anandimvera nthawi ijanso.

20. Ndipo Yehova aliakwiya kwambiri ndi Aroni kumuononga; koma ndinampempherera Aroni nthawi yomweyo.

21. Ndipo ndinatenga cimo lanu, mwana wa ng'ombe mudampangayo, ndi kumtentha ndi moto, ndi kumphwanya, ndi kumpera bwino kufikira atasalala ngati pfumbi; ndipo ndinataya pfumbi lace m'mtsinje wotsika m'phirimo.

22. Ku Tabera, ndi ku Masa, ndi ku Kibiroti Hatava, munautsanso mkwiyo wa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 9