Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 9:1-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Imvani Israyeli; mulikuoloka Yordano lero lino, kulowa ndi kulandira amitundu akuru ndi amphamvu akuposa inu, midzi yaikuru ndi ya malinga ofikira kuthambo,

2. anthu akuru ndi atalitali, ana a Aanaki, amene muwadziwa, amene munamva mbiri yao, ndi kuti, Adzaima ndani pamaso pa ana a Anaki?

3. Potero mudziwe lero lino, kuti Yehova Mulungu wanu ndiye amene aoloka pamaso panu ngati moto wonyeketsa; iye adzawaononga, iye adzawagwetsa pamaso panu; potero mudzawapitikitsa, ndi kuwaononga msanga, monga Yehova analankhula ndi inu.

4. Musamanena mumtima mwanu, atawapitikitsa pamaso panu Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Cifukwa ca cilungamo canga Yehova anandilowetsa kudzalandira dziko ili; pakuti Yehova awapitikitsa pamaso panu cifukwa ca zoipa za amitundu awa.

5. Simulowa kulandira dziko lao cifukwa ca cilungamo canu, kapena mtima wanu woongoka; koma Yehova Mulungu wanu awapitikitsa pamaso panu cifukwa ca zoipa za amitundu awa, ndi kuti akhazikitse mau amene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo.

6. Potero mudziwe, kuti Yehova Mulungu wanu sakupatsani dziko ili lokoma mulilandire, cifukwa ca cilungamo canu; pakuti inu ndinu mtundu wa aathu opulukira.

7. Kumbukilani, musamaiwala, kuti munakwiyitsa Yehova Mulungu wanu m'cipululu; kuyambira tsikuli munaturuka m'dziko la Aigupto, kufikira munalowa m'malo muno munapiktsana ndi Yehova.

8. M'Horebe momwe munautsa mkwiyo wa Yehova; ndipo Yehova anakwiya nanu kukuonongani.

9. Muja ndinakwera m'phiri kukalandira ma gome amiyala, ndiwo magome a cipangano cunene Yehova anapangana ndi inu, ndinakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku; osadya mkate osamwa madzi.

10. Ndipo Yehova anapereka kwa ine magome awiri amiyala, olembedwa ndi cala ca Mulungu; ndipo panalembedwa pamenepo monga mwa mau onse amene Yehova adanena ndi inu m'phirimo, ali pakati pa moto, tsiku lakusonkhana.

11. Ndipo kunali, atatha masiku makumi anai usana ndi usiku, kuti Yehova anandipatsa magome awiriwo amiyala, ndiwo magome a cipangano,

12. Ndipo Yehova anati kwa ine, Uka, fulumira kutsika kuno popeza anthu ako unawaturutsa m'Aigupto wa anadziipsa; anapatuka msanga m'njira ndinawalamulirayi; anadzipangira fano loyenga.

13. Yehova ananenanso ndi ine, ndi kuti, Ndapenya anthu awa, taona, awa ndi anthu opulukira;

14. undileke, ndiwaononge, ndi kufafaniza dzina lao pansi pa thambo; ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu wa anthu wamphamvu ndi waukuru woposa iwo.

15. Pamenepo ndinatembenuka ndi kutsika m'phiri, ndi phirilo linatentha ndi moto; ndi magome awiri a cipangano anali m'manja mwanga.

16. Ndipo ndinapenya, taonani, mudacimwira Yehova Mulungu wanu; mudadzipangira mwana wa ng'ombe woyenga; mudapatuka msanga m'njira imene Yehova adalamulira inu.

17. Pamenepo ndinagwira magome awiriwo, ndi kuwataya acoke m'manja anga awiri, ndi kuwaswa pamaso panu.

18. Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova, monga poyamba paja, masiku makumi anai usana ndi usiku, osadya mkate osamwa madzi, cifukwa ca macimo anu onse mudacimwa, ndi kucita coipaco pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wace.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 9