Musamanena mumtima mwanu, atawapitikitsa pamaso panu Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Cifukwa ca cilungamo canga Yehova anandilowetsa kudzalandira dziko ili; pakuti Yehova awapitikitsa pamaso panu cifukwa ca zoipa za amitundu awa.