Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 7:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamene Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene mumkako kulilandira likhale lanu lanu, ndipo atakataya amitundu ambiri pamaso panu, Ahiti, ndi Agirigazi, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, mitundu isanu ndi iwiri yaikuru ndi yamphamvu yoposa inu;

2. nakawapereka Yehova Mulungu wanu pamaso panu, ndipo mukawakanthe; pamenepo muwaononge konse; musapangana nao pangano, kapena kuwacitira cifundo.

3. Ndipo musakwatitsane nao; musampatsemwana wace wamwamuna mwana wanu wamkazi, kapena kutenga mwana wace wamkazi akhale wa mwana wanu wamwamuna.

4. Popeza adzapatutsa mwana wanu aleke kunditsata Ine, kuti atumikire milungu yina; potero Yehova adzapsa mtima pa inu, ndipo adzakuonongani msanga.

5. Koma muzicita nao motero: mukapasule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao, ndi kutentha mafano ao osema ndi moto.

6. Pakuti inu ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu; Yehova Mulungu wanu anakusankhani, mukhale mtundu wa pa wokha wa iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu akukhala pa nkhope ya dziko.

7. Yehova sanakondwera nanu, ndi kukusankhani cifukwa ca kucuruka kwanu koposa mitundu yonse yina ya anthu, kapena kucepera kwanu;

8. koma Yehova anakuturutsani ndi dzanja lamphamvu, ndi kukuombolani m'nyumba ya akapolo, m'dzanja la Farao mfumu ya Aigupto, cifukwa Yehova akukondani, ndi cifukwa ca kusunga lumbiro lija analumbirira makolo anu.

9. Cifukwa cace dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga cipangano ndi cifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ace, kufikira mibadwo zikwi.

10. Ndipo awabwezera onse akudana ndi iye, pamaso pao, kuwaononga; sacedwa naye wakudana ndi iye, ambwezera pamaso pace.

11. Potero muzisunga malamulo, ndi malemba, ndi maweruzo, amene ndikuuzani lero kuwacita.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 7