Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 5:20-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Usamnamizire mnzako.

21. Usasirire mkazi wace wa mnzako; usakhumbe nyumba yace ya mnzako, munda wace, kapena wanchito wace wamwamuna, kapena wanchito wace wamkazi, ng'ombe yace, kapena buru wace, kapena kanthu kali konse ka mnzako.

22. Yehova ananena mau awa kwa msonkhano wanu wonse, m'phirimo ali pakati pa moto, pamtambo, pamdima bii, ndi mau akuru; osaonjezapo kanthu. Ndipo anawalembera pa magome awiri amiyala, nandipatsa awa.

23. Ndipo kunali, pamene munamva liu loturuka pakati pa mdima, potentha phiri ndi moto, munayandikiza kwa ine, ndiwo mafumu onse a mapfuko anu ndi akuru anu;

24. ndipo munati, Taonani, Yehova Mulungu wathu anationetsa ulemerero wace, ndi ukuru wace, ndipo tidamva liu lace ali pakati pa mote; tapenya lero lino kuti Mulungu anena ndi munthu, ndipo akhala ndi moyo.

25. Ndipo tsopano tiferenji? popeza mote waukuru uwu udzatitha. Tikaonjeza kumva mau a Yehova Mulungu wathu, tidzafa.

26. Pakuti ndaniyo, wa zamoyo zonse adamva mau a Mulungu wamoyo wakunena ali pakati pa moto, monga ife, nakhala ndi moyo?

27. Yandikizani inu, ndi kumva zonse Yehova Mulungu wathu adzati; ndipo inu munene ndi ife zonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanena ndi inu; ndipo ife tidzazimva ndi kuzicita.

28. Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, pamene munanena ndi ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Ndidamva mau a kunena kwao kwa anthu awa, amene ananena ndi iwe; cokoma cokha cokha adanenaci.

29. Ha! mwenzi akadakhala nao mtima wotere wakundiopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti ciwakomere iwo ndi ana ao nthawi zonse!

30. Muka, nuti nao, Bwererani ku mahema anu.

31. Koma iwe, uime kuno ndi Ine, ndinene ndi iwe malamulo onse, ndi malemba, ndi maweruzo, amene uziwaphunzitsa, kuti awacite m'dziko limene ndiwapatsa likhale lao lao.

32. Potero muzisamalira kucita monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani; musamapatuka kulamanzere kapena kulamanja.

33. Muziyenda m'njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani, kuti mukakhale ndi moyo, ndi kuti cikukomereni, ndi kuti masiku anu acuruke m'dziko limene mudzakhala nalo lanu lanu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 5