Yehova ananena mau awa kwa msonkhano wanu wonse, m'phirimo ali pakati pa moto, pamtambo, pamdima bii, ndi mau akuru; osaonjezapo kanthu. Ndipo anawalembera pa magome awiri amiyala, nandipatsa awa.