Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 31:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Yehova akadzawapereka pamaso panu, muziwacitira monga mwa lamulo lonse ndakuuzani.

6. Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamacita mantha, kapena kuopsedwa cifukwa ca iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; iye sadzakusowani, kapena irukusiyani.

7. Ndipo Mose anaitana Yoswa, nati naye pamaso pa Israyeli wonse, Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao anthu awa m'dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kuwapatsa ilo; ndipo iwe udzawalandiritsa ilo.

8. Ndipo Yehova, iye ndiye amene akutsogolera; iye adzakhala ndi iwe, iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamacita mantha, usamatenga nkhawa.

9. Ndipo Mose analembera cilamulo ici, nacipereka kwa ansembe, ana a Levi, akunyamula likasa la cipangano la Yehova, ndi kwa akuru onse a Israyeli,

10. Ndipo Mose anawauza, ndi kuti, Pakutha pace pa zaka zisanu ndi ziwiri, pa nyengo yoikika ya m'caka cakulekerera, pa madyerero a misasa;

11. pakufika Israyeli wonse kuoneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo amene adzasankha, muzilalikira cilamulo ici pamaso pa Israyeli wonse, m'makutu mwao.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 31