Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 31:18-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Koma Ine ndidzabisatu nkhope yanga tsiku lija cifukwa ca zoipa zonse adazicita; popeza anadzitembenukira milungu yina.

19. Ndipo tsopano mudzilemberere nyimbo iyi, ndi kuphunzitsa ana a Israyeli iyi: mulike m'kamwa mwao, kuti nyimbo iyi indicitire mboni yotsutsa ana a Israyeli.

20. Pakuti nditakalowetsa awa m'dziko limene ndinalumbirira makolo ao, moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; ndipo atadya nakhuta, nanenepa, pamenepo adzatembenukira milungu yina, ndi kuitumikira, ndi kundipeputsa Ine, ndi kutyola cipangano canga.

21. Ndipo kudzakhala, zitawafikira zoipa ndi zobvuta zambiri, nyimbo iyi idzacita mboni pamaso pao; popeza siidzaiwalika m'kamwa mwa mbeu zao; popeza ndidziwa zolingirira zao azicita lero lino, ndisanawalowetse m'dziko limene ndinalumbira.

22. Potero Mose analembera nyimboyi tsiku lomweli, naiphunzitsa ana a Israyeli.

23. Ndipo anauza Yoswa mwana wa Nuni, nati, Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao ana a Israyeli m'dziko limene ndinawalumbirira: ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 31