Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 3:3-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Potero Yehova Mulungu wathu anaperekanso m'manja mwathu Ogi mfumu ya Basana, ndi anthu ace onse, ndipo tinamkantha kufikira sanamtsalira ndi mmodzi yense.

4. Ndipo muja tinalanda midzi yace yonse; kunalibe mudzi sitinaulanda m'manja mwao, midzi makumi asanu ndi limodzi, dera lonse la Arigobi, dziko la Ogi m'Basana.

5. Yonseyi ndiyo midzi yozinga ndi malinga atali, zitseko, ndi mipiringidzo; pamodzi ndi midzi yambirimbiri yopanda malinga.

6. Ndipo tinaiononga konse, monga umo tinacitira Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi kuononga konse midzi yonse, amuna, akazi ndi ana.

7. Koma zoweta zonse ndi zofunkha za m'midzi, tinadzifunkhira tokha.

8. Ndipo muja tinalanda dziko m'manja mwa mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordano, kuyambira mtsinje wa Arinoni kufikira phiri la Herimoni;

9. (Asidoni alicha Herimoni Sirioni, koma Aamori alicha Seniri);

10. midzi yonse ya kucidikha, ndi Gileadi lonse, ndi Basana lonse kufikira ku Saleka ndi Edrei, midzi ya dziko la Ogi m'Basana.

11. (Pakuti Ogi mfumu ya Basana anatsala yekha wa iwo otsalira Arefai; taonani, kama wace ndiye kama wacitsulo; sukhala kodi m'Raba wa ana a Amoni? utali wace mikono isanu ndi inai, kupingasa kwace mikono inai, kuyesa mkono wa munthu.)

12. Ndipo dziko ili tinalilanda muja; kuyambira ku Aroeri, wa ku mtsinje wa Arinoni, ndi dera lina la ku mapiri a Gileadi, ndi midzi yace, ndinapatsa Arubeni ndi Agadi.

13. Ndi cotsalira ca Gileadi, ndi Basana lonse, dziko la Ogi, ndinapatsa pfuko la hafu la Manase; dziko lonse la Arigobi, pamodzi ndi Basana. (Ndilo lochedwa dziko la Arefai.

14. Yairi mwana wa Manase analanda dziko lonse la Arigobi, kufikira malire a Agesuri ndi Amaakati; nalicha dzina lace, Basana Haroti Yairi, kufikira lero lino.)

15. Ndipo ndinampatsa Makiri Gileadi.

16. Koma ndinapatsa Arubeni ndi Agadi kuyambira ku Gileadi kufikira ku mtsinje wa Arinoni, pakati pa cigwa ndi malire ace, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;

17. ndi cidikha, ndi Yordano ndi malire ace, kuyambira ku Kinerete kufikira ku nyanja ya kucidikha, ndiyo Nyanja ya Mcere, patsinde pa Pisiga, kum'mawa.

18. Ndipo ndinauza inu muja, ndi kuti, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili likhale lanu lanu, muoloke, amuna onse amphamvu obvala zida zao, pamaso pa abale anu ana a Israyeli.

19. Koma akazi anu, ndi ana anu, ndi zoweta zanu, (ndidziwa muli nazo zoweta zambiri), zikhale m'midzi yanu imene ndinakupatsani;

20. kufikira Yehova atapumulitsa abale anu, monga anapumulitsa inu, nalandira iwonso dziko limene Yehova Mulungu wanu awapatsa tsidya lila la Yordano; pamenepo mudzabwerera munthu yense ku colowa cace, cimene ndinakupatsani.

21. Ndipo ndinauza Yoswa muja, ndi kuti, Maso ako anapenya zonse Yehova Mulungu wanu anawacitira mafumu awa awiri; momwemo Yehova adzacitira maufumu onse kumene muolokerako.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 3