Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 28:5-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Zidzakhala zodala mtanga wanu, ndi coumbiramo mkate wanu.

6. Mudzakhala odala polowa inu, mudzakhala odala poturuka inu.

7. Yehova adzakantha adani anu akukuukirani; adzakudzerani njira imodzi, koma adzathawa pamaso panu njira zisanu ndi ziwiri.

8. Yehova adzakulamulirani dalitso m'nkhokwe zanu, ndi m'zonse muturutsirako dzanja lanu; ndipo adzakudalitsani m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani,

9. Yehova adzakukhazikirani yekha mtundu wa anthu wopatulika, monga anakulumbirirani; ngati mudzasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zace.

10. Ndipo anthu onse a pa dziko lapansi adzaona kuti akuchulani dzina la Yehova; nadzakuopani.

11. Ndipo Yehova adzakucurukitsirani zokoma, m'zipatso za thupi lanu, ndi m'zipatso za zoweta zanu, ndi m'zipatso za nthaka yanu, m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo,

12. Yehova adzakutsegulirani cuma cace cokoma, ndico thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yace, ndi kudalitsa nchito zonae za dzanja lanu; ndipo mudza kongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.

13. Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mcira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwacita;

14. osapatukira mau ali onse ndikuuzani lero, kulamanja, kapena kulamanzere, kutsata milungu yina kuitumikira.

15. Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kucita malamulo ace onse ndi malemba ace amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani,

16. Mudzakhala otembereredwa m'mudzi, ndi otembereredwa pabwalo.

17. Zidzakhala zotembereredwa mtanga wanu ndi coumbiramo mkate wanu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 28