Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 28:11-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo Yehova adzakucurukitsirani zokoma, m'zipatso za thupi lanu, ndi m'zipatso za zoweta zanu, ndi m'zipatso za nthaka yanu, m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo,

12. Yehova adzakutsegulirani cuma cace cokoma, ndico thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yace, ndi kudalitsa nchito zonae za dzanja lanu; ndipo mudza kongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.

13. Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mcira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwacita;

14. osapatukira mau ali onse ndikuuzani lero, kulamanja, kapena kulamanzere, kutsata milungu yina kuitumikira.

15. Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kucita malamulo ace onse ndi malemba ace amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani,

16. Mudzakhala otembereredwa m'mudzi, ndi otembereredwa pabwalo.

17. Zidzakhala zotembereredwa mtanga wanu ndi coumbiramo mkate wanu.

18. Zidzakhala zotembereredwa zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.

19. Mudzakhala otembereredwa polowa inu, ndi otembereredwa poturuka inu.

20. Yehova adzakutumizirani temberero, cisokonezeko, ndi kudzudzula monsemo mukaturutsa dzanja lanu kucita kanthu, kufikira mwaonongeka, kufikira mwatayika rosanga, cifukwa ca zocita inu zoipa, zimene wandisiya nazo,

21. Yehova adzakumamatiritsani mliri kufikira akakuthani kukucotsani kudziko, kumene mupitako kulilandira.

22. Yehova adzakukanthani ndi nthenda yoondetsa ya cifuwa, ndi malungo, ndi cibayo, ndi kutentha thupi, ndi lupanga, cinsikwi ndi cinoni; ndipo zidzakutsatani kufikira mwatayika.

23. Ndipo thambo lanu la pamwamba pamutu panu lidzakhala ngati mkuwa, ndi dziko liri pansi panu ngati citsulo.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 28