Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 25:6-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo kudzali, kuti woyamba kubadwa amene adzambala, adzalowa dzina lace la mbale wace wafayo, kuti dzina lace lisafafanizidwe m'Israyeli.

7. Ndipo ngati mwamunayo safuna kutenga mkazi wa mbale wace, mkazi wa mbale waceyo azikwera kumka kucipata, kwa akuru, ndi kuti, Mbale wa mwamuna wanga akana kuutsira mbale wace dzina m'Israyeli; safuna kundicitira ine zoyenera mbale wa mwamuna.

8. Pamenepo akuru a mudzi wace amuitane, ndi kulankhula naye; ndipo akaimirira ndi kuti, Sindifuna kumtenga;

9. pamenepo mkazi wa mbale wace azimyandikiza pamaso pa akuru, nacotse nsapato yace ku ph zi la mwamunayo, ndi kumthira malobvu pankhope pace, ndi kumyankha ndi kuti, Atere naye mwamuna wosamanga nyumba ya mbale wace.

10. Ndipo azimucha dzina lace m'Israyeli, Nyumba ya uje anamcotsa nsapato.

11. Akalimbana wina ndi mnzace, nakayandikiza mkazi wa winayo kulanditsa mwamuna wace m'dzanja la wompandayo, nakaturutsa dzanja lace, ndi kumgwira kudzibvalo;

12. pamenepo muzidula dzanja lace; diso lanu lisamcitire cifundo.

13. Musamakhala nayo m'thumba mwanu miyala ya miyeso iwiri, waukuru ndi waung'ono.

14. Musamakhala nayo m'nyumba yanu miyeso ya efa yosiyana, waukuru ndi waung'ono.

15. Muzikhala nao mwala wa muyeso wofikira ndi woyenera; mukhale nao muyeso wa efa wofikira ndi woyenera; kuti masiku anu acuruke m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

16. Pakuti onse akucita zinthu izi, onse akucita cisalungamo, Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.

17. Kumbukilani cocitira inu Amaleki panjira, poturuka inu m'Aigupto;

18. kuti anakomana ndi inu panjira, nakantha onse ofok a akutsala m'mbuyo mwanu, pakulema ndi kutopa inu; ndipo sanaopa Mulungu,

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 25