Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 24:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Munthu akatenga mkazi akhale wace, kudzali, ngati sapeza ufulu pamaso pace, popeza anapeza mwa iye kanthu kosayenera, amlembere kalata wa cilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lace, ndi kumturutsa m'nyumba mwace.

2. Ndipo ataturuka m'nyumba mwace, amuke nakhale mkazi wa mwamuna wina.

3. Ndipo akamuda mwamuna waciwiriyo, nakamlemberanso kalata wa cilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lace, nakamturutsa m'nyumba mwace; kapena akamwalira mwamuna wotsirizayo, amene anamtenga akhale mkazi wace;

4. pamenepo mwamuna woyamba anamcotsayo sangathe kumtenganso akhale mkazi wace, atadetsedwa iye; pakuti ici ndi conyansa pamaso pa Yehova; ndipo usamacimwitsa dziko, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colandira canu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 24