Munthu akatenga mkazi akhale wace, kudzali, ngati sapeza ufulu pamaso pace, popeza anapeza mwa iye kanthu kosayenera, amlembere kalata wa cilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lace, ndi kumturutsa m'nyumba mwace.