Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 2:9-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Pamenepo tinatembenuka ndi kudzera njira ya cipululu ca Moabu. Ndipo Yehova anati kwa ine, Usabvuta Moabu, kapena kuutsana naye nkhondo; popeza sindidzakupatsako dziko lace likhale lako lako; pakuti ndinapatsa ana a Loti Ari likhale lao lao.

10. (Aemi anakhalamo kale, ndiwo anthu akuru, ndi ambiri, ndi atalitali, ngati Aanaki.

11. Anawayesa iwonso Arefai, monga Aanaki; koma Amoabu awacha Aemi.

12. Ndipo Ahori anakhala m'Seiri kale, koma ana a Esau analanda dziko lao, nawaononga pamaso pao, nakhala m'malo mwao; monga Israyeli anacitira dziko lace lace, limene Yehova anampatsa.)

13. Ukani tsopano, olokani mtsinje wa Zeredi. Ndipo tinaoloka mtsinje wa Zeredi.

14. Ndipo masiku amene tinayenda kucokera ku Kadesi Barinea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m'cigono, monga Yehova adawalumbirira.

15. Komanso dzanja la Yehova linatsutsana nao, kuwaononga m'cigono, kufikira adawatha.

16. Ndipo kunali, atatha kufa amuna onse ankhondo mwa anthu,

17. Yehova ananena ndi ine, ndi kuti,

18. Lero lomwe utumphe malire a Moabu, ndiwo Ari.

19. Ndipo pamene uyandikiza popenyana ndi ana a Amoni, usawabvuta, kapena kuutsana nao; popeza sindidzakupatsako dziko la ana a Amoni likhale lako lako; popeza ndinapatsa ana a Loti ili likhale lao lao.

20. (Ilinso aliyesa dziko la Arefai; Arefai anakhalamo kale; koma Aamoni awacha Azamzumi;

21. ndiwo anthu akuru, ndi ambiri, ndi atalitali, monga Aanaki; koma Yehova anawaononga pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 2