Ndipo pamene uyandikiza popenyana ndi ana a Amoni, usawabvuta, kapena kuutsana nao; popeza sindidzakupatsako dziko la ana a Amoni likhale lako lako; popeza ndinapatsa ana a Loti ili likhale lao lao.