Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 15:2-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Cilekereroco ndici: okongoletsa onse alekerere cokongoletsa mnansi wace; asacifunse kwa mnansi wace, kapena mbale wace; popeza analalikira cilekerero ca Yehova.

3. Muyenera kucifunsa kwa mlendo; koma canu ciri conse ciri ndi mbale wanu, dzanja lanu licilekerere;

4. ndiko kuti pasakhale waumphawi mwa inu; pakuti Yehova adzakudalitsani kwambiri m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colowa canu canu;

5. cokhaci mumvere cimverere mau a Yehova Mulungu wanu, kuti musamalire kucita malamulo awa onse amene ndikuuzani lero lino.

6. Popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani, monza ananena nanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha; nimudzacita ufumu pa amitundu ambiri, koma iwo sadzacita ufumu pa inu.

7. Akakhala ndi inu munthu waumphawi, ndiye wilia wa abale anu, m'umodzi wa midzi yanu, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musakhakala mtima wanu, kapena kuumitsa dzanja lanu kukaniza mbale wanu waumphawi;

8. koma muzimtansira dzanjalanundithu ndi kumkongoletsa ndithu zofikira kusowa kwace, monga umo amasowa.

9. Dzicenjerani, mungakhale mau opanda pace mumtima mwanu, ndi kuti, Cayandika caka cacisanu ndi ciwiri, caka ca cilekerero; ndipo diso lanu lingaipire mbale wanu waumphawi, osampatsa kanthu; ndipo iye angalirire inu kwa Yehova; ndipo mwa inu mungakhale cimo.

10. Muzimpatsa ndithu, osawawa mtima wanu pompatsa; popeza, cifukwa ca ici Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mu nchito zanu zonse, ndi m'zonse muikapo dzanja lanu.

11. Popeza waumphawi salekana m'dziko, cifukwa cace ndikuuzani ndi kuti, Dzanja lanu mulitansire ndithu mbale wanu, ndi ozunzika anu, ndi aumphawi anu, a m'dziko mwanu.

12. Mukagula mbale wanu, Mhebri wamwamuna kapena Mhebri wamkazi, ndipo adzakutumikira zaka zisanu ndi cimodzi; koma caka cacisanu ndi ciwiri umlole acoke kwanu waufulu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 15