Popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani, monza ananena nanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha; nimudzacita ufumu pa amitundu ambiri, koma iwo sadzacita ufumu pa inu.